Joshua 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabanja otsala a Manase amene adapatsidwanso dziko ndi aŵa: Abiyezere, Heleki, Asiriele, Sekemu, Hefere ndi Semida. Ameneŵa ndiwo zidzululu za Manase, mwana wa Yosefe, komanso ndiwo amene anali eni mbumba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana amuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mabanja ena otsala a fuko la Manase amene analandira dziko ndi awa: Abiezeri, Heleki, Asirieli, Sekemu, Heferi ndi Semida. Izi ndi zidzukulu zina zazimuna za Manase mwana wa Yosefe ndiponso eni mbumba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriyeli, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana amuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao.