Joshua 17:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali Zelofehadi mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Zelofehadiyo analibe mwana wamwamuna ndi mmodzi yemwe, koma aakazi okhaokha. Maina a ana aakaziwo ndi aŵa: Mahala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri mwana wa Manase. Iyeyu analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha ndipo mayina awo ndi awa: Mahila, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Tselofekadi, mwana wa Hefere, mwana wa Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.