Joshua 17:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa adabwera kwa Eleazara wansembe, nafikanso kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri, ndipo adati, “Chauta adalamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse gawo lina la dziko ngati choloŵa chathu.” Motero iwowo, pamodzi ndi abale a bambo wao, adapatsidwa dziko kuti likhale lao potsata zimene Chauta adalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapita kwa Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri ndipo anati: “Yehova analamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse cholowa chathu.” Choncho iwowo pamodzi ndi abale a abambo awo anawapatsa dera lina la dzikolo kuti likhale monga mwa lamulo la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazare wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse colowa pakati pa abale athu; cifukwa cace anawapatsa monga mwa lamulo La Yehova, colowa pakati pa abale a atate wao.