Joshua 17:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
popeza kuti ana aakazi a Manase ndi ana ake aamuna, onsewo adalandira magawo ao. Dziko la Giliyadi lidapatsidwa kwa otsala mwa zidzukulu za Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza ana akazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake amuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa ana aakazi a fuko la Manase analandira cholowa chawo pakati pa ana aamuna. Dziko la Giliyadi linali dziko la zidzukulu zonse za Manase.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza ana akazi a Manase adalandira colowa pakati pa ana ace amuna; ndi dziko la Gileadi linakhala la ana a Manase otsala.