Joshua 17:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko la Manase malire ake adachokera ku Asere, ndipo adakafika ku Mikimetati kuvuma kwa Sekemu. Tsono malire adapita kumwera kuloza kwa anthu a ku Entapuwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malire a dziko la Manase anayambira ku Aseri, ndipo anakafika ku Mikimetati kummawa kwa Sekemu. Tsono malire anapita kummwera kuloza kwa anthu a ku Eni-Tapuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire a Manase anayambira ku Aseri, kumka ku Mika-metatu, wokhala cakuno ca Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapua.