Joshua 17:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono malire ake adatsikira ku kamtsinje ka Kana. Mizinda yakumwera kwa kamtsinje kameneka inali ya fuko la Efuremu, ngakhale inali m'dziko la Manase. Malire a dziko la Manase adalambalala chakumpoto kwa kamtsinjeko, nakalekezera ku nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efuremu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndi matulukiro ake anali kunyanja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo malire ake anapitirira kummwera mpaka ku mtsinje wa ku Kana. Mizinda ya kummwera kwa mtsinjewo inali ya fuko la Efereimu ngakhale kuti inali mʼdziko la Manase. Malire a fuko la Manase anapita kumpoto kwa mtsinje wa Kana ndi kukathera ku Nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efraimu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndimaturukiro ace anali kunyanja;