Joshua 18:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yoswa adachita maere, naŵapemphera nzeru kwa Chauta. Ndipo fuko lililonse la Aisraele adalipatsa gawo la dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israyeli dziko, monga mwa magawo ao.