Joshua 18:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono malirewo adaloza ku Luzi, ndi kutsata mbali ya phiri loti Luzi, (lotchedwanso Betele). Tsono adatsikira ku Ataroti-Adara, kubzola phiri lili kumwera kwa Betehoroni wakunsi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire anapitirirapo kunka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Betele, kumwera; ndi malire anatsikira kunka ku Ataroti-Adara, kuphiri lokhala kumwera kwa Betehoroni wa kunsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire anapitirirapo kumka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Beteli, kumwela; ndi malire anatsikira kumka ku Atarotu-adara, ku phiri lokhala kumwela kwa Betihoroni wa kunsi.