Joshua 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo malirewo adaloŵanso kwina, nalunjika kumwera kuchokera kuzambwe kwake kwa phiri limene limayang'anana ndi Betehoroni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati-Baala (wotchedwanso Kiriyati-Yeyarimu), mzinda wa fuko la Yuda. Ameneŵa ndiwo anali malire akuzambwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kumka kumwela, kucokera ku phiri pokhala patsogolo pa Beti-horoni, kumwela kwace; ndi maturukiro ace anali ku Kiriyatibaala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.