Joshua 18:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malire akumwera adayambira pamphepete penipeni pa Kiriyati-Yearimu, napita kuzambwe mpaka kukafika ku Akasupe a ku Nefutowa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbali ya kumwera inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; natuluka malire kunka kumadzulo, natuluka kunka ku chitsime cha madzi a Nefitowa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbali ya kumwela inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; naturuka malire kumka kumadzulo, naturuka kumka ku citsime ca madzi a Nefitoa;