Joshua 18:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatsikira m'mphepete mwa phiri limene limayang'anana ndi chigwa cha Benihinomu, cha kumpoto kwake kwa chigwa cha Arefaimu. Adapita chakumwera kubzola chigwa cha Hinomu, kumwera kwa chitunda cha Ayebusi, moyang'ana ku Enirogele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m'chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
natsikira malire kumka polekezera phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca mwana wa Hinomu, ndico ca m'cigwa ca Refai kumpoto; natsikira ku cigwa ca Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwela, natsikira ku Enirogeli;