Joshua 18:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono malire adakhota, naloŵa kumpoto ku Enisemesi ndi kubzola mpaka kukafika ku Geliloti, kuyang'anana ndi pokwerera pa Aduminu. Atatero malirewo adatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nalembedwa kunka kumpoto, natuluka ku Enisemesi, natuluka ku Geliloti, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumimu; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nalembedwa kumka kumpoto, naturuka ku Eni-semesi, naturuka ku Gelilotu, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumi; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;