Joshua 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapitiriranso kumpoto kwa chitunda cha Betehogila, ndipo adakathera chakumpoto ku mathiriro a mtsinje wa Yordani m'Nyanja Yakufa, kumwera kwake kwenikweni kwa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napitirira malire kunka ku mbali ya Betehogila kumpoto; ndi matulukiro ake a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mchere; pa kulekezera kwa kumwera kwa Yordani; ndiwo malire a kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napitirira malire kumka ku mbali ya Beti-hogila kumpoto; ndi maturukiro ace a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mcere; pa kulekezera kwa kumwela kwa Yordano; ndiwo malire a kumwera.