Joshua 18:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsinje wa Yordani ndiye udachita malire kuvuma kwake. Ameneŵa ndiwo anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire ake mbali ya kum'mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa. Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malireace mbali ya kum'mawa ndiwo Yordano, ndico colowa ca ana a Benjamini, kunena za malire ace pozungulira pace, monga mwa mabanja ao.