Joshua 18:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zela, Haelefe, Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu), Gibea ndi Kiriyati-Yearimu. Yonse inalipo 14, pamodzi ndi midzi yake. Dziko limeneli ndilo limene mabanja a Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Zela, Elefi, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibeati ndi Kiriyati; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi miraga yace, Ndico colowa ca ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.