Joshua 18:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tandipatsani amuna atatu a fuko lililonse. Ameneŵa ndiŵatuma kuti akayendere dziko lonselo, ndipo alembe bwino magawo ake onse, kuti tithandizidwe poligaŵa. Atatero, abwererenso kuno kwa ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzifunire amuna, pfuko liri lonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa colowa cao; nabwereoso kwa ine.