Joshua 18:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi okha sadzalandira nao gawo la dzikolo, popeza kuti gawo lao ndi kutumikira Chauta pa unsembe. Fuko la Gadi ndi la Rubeni ndi theka la fuko la Manase adalandira kale dziko lao kuvuma kwa Yordani. Mose, mtumiki wa Chauta, ndiye adaŵapatsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum'mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo colowa cao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi pfuko la Manase logawika pakati adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano kum'mawa, cimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.