Joshua 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthuwo adakaliyendera dziko lonselo, nalemba bwino m'buku za dzikolo. Adagaŵa dzikolo magawo asanu ndi aŵiri, ndipo adalembanso mndandanda wa midzi yonse. Atatero adabwerera kwa Yoswa ku zithando ku Silo kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yace, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku cigono ku Silo.