Joshua 19:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabanja a Simeoni adalandiranso gawo lao, Yoswa atachita maere kachiŵiri. Dziko lake linali m'kati mwenimweni mwa dziko la mabanja a Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maere aciwiri anamturukira Simeoni, pfuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi colowa cao cinali pakati pa colowa ca ana a Yuda.