Joshua 19:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono malirewo adakhotera ku Rama, nakafika mpaka ku Tiro, mzinda wozingidwa ndi linga. Pamenepo adakhoteranso ku Hosa, nkukatulukira ku nyanja, m'dera la Akizibu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumudzi wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nazungulira malice kumka ku Rama, ndi ku mudzi wa linga la Turo; nazungulira malire kumka ku Hosa; ndi maturukiro ace anali kunyanja, kucokera ku Hebeli mpaka ku Akizibu;