Joshua 19:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu a fuko la Dani adalandidwa dziko lao, adapita nakathira nkhondo Lesemu, nagonjetseratu ndi kuwononga adani onse. Tsono atatero, adalanda mzindawo, nakhazikika kumeneko. Ndipo adasintha dzina la mzindawo kuti likhale Dani, pakuti limeneli linali dzina la kholo lao Dani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma malire a ana a Dani anaturuka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, naucha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.