Joshua 19:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele atatha kugaŵana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, adamgaŵirako Yoswa mwana wa Nuni dera lina la dzikolo kuti likhale choloŵa chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atatha kuligawa dziko likhale colowa cao monga mwa malire ace, ana a Israyeli anapatsa Yoswa mwana wa Nuni colowa pakati pao;