Joshua 19:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potsata zimene Chauta adalamula, adampatsako mzinda wa Timnati-Sera umene Yoswayo mwiniwake adaapempha, umene unali m'dziko la Efuremu lamapiri lija. Kumeneko ndiko kumene adamanga mzinda wake, nakhazikika komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mudziwo nakhala m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timinatisera, ku mapiri a Efraimu; ndipo anamangamudziwonakhala m'mwemo.