Joshua 19:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, pamodzi ndi atsogoleri amabanja a Aisraele, ndiwo amene adagaŵa dziko limeneli zigawozigawo, pochita maere pamaso pa Chauta. Ndipo ankachita zimenezi ku Silo, ku chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano chija. Choncho adamaliza kuligaŵa dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, zikhale zao zao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la cihema cokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.