Joshua 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gawo la Simeoni lidatapidwa ku gawo la Yuda, popeza kuti gawo la Yuda lidaali lalikulu kwambiri. Choncho choloŵa cha Simeoni chidatapidwa pa choloŵa cha Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.