Joshua 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde, tamva m'mene Chauta adaphwetsera Nyanja Yofiira inu mukufika, m'mene munkatuluka ku Ejipito. Tamvanso m'mene mudakanthira mafumu aŵiri a Aamori, Sihoni ndi Ogi, kuvuma kwa Yordani kuja. Mudakantha ndi magulu ao ankhondo omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m'Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudaruruka m'Aigupto; ndi cija munacitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordano, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.