Joshua 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano mulumbire pamaso pa Chauta kuti mudzasunga zimene mulonjeze, ndipo kuti mudzachitira chifundo banja langa, monga momwe ndakusamalirani inu, ndipo munditsimikizire kwenikweni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mulumbire pamaso pa Yehova ndi kundipatsa chizindikiro choti mudzachitadi zimene mwalonjeza, kuti monga inu ndakuchitirani chifundo, inunso mudzachitira chifundo a pa banja la abambo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakucitirani cifundo, kuti inunso mudzacitira cifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa cizindikilo coona,