Joshua 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anali ataŵauza kuti, “Pitani mudzere kumapiriko, kuti otumidwa ndi mfumu aja angakupezeni. Papite masiku atatu mukubisalabe, mpaka iwowo atachokako. Zitatero tsono, mungathe kumapita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Pitani ku mapiri kuti okuthamangiraniwo asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu mpaka iwo atabwerera, ndipo kenaka muzikapita kwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu.