Joshua 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mvetsa tsono. Tikadzaloŵa, iweyo udzamange chingwe chofiirachi pawindo pomwe watitulutsirapa. Bambo wako, mai wako, abale ako ndi onse a m'banja la bambo wako, adzakhale m'nyumba mwako muno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
tikadzalowa mʼdzikoli, iwe udzamangirire kansalu kofiira pa zenera limene unatitulutsira, ndi kusonkhanitsa abambo ako, amayi ako, abale ako ndi banja lako lonse mʼnyumba muno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga cingwe ici cofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako nui abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.