Joshua 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mfumuyo idatuma anthu kwa Rahabu kukamuuza kuti, “Anthu amene ali m'nyumba mwakowo abwera kudzazonda dziko lonseli, tsono atulutse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabe kuti, “Atulutse anthu amene abwera ku nyumba kwakowo chifukwa iwo abwera kuti adzazonde dzikoli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Turutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.