Joshua 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamenepo mkaziyo nkuti ataŵatenga amuna aŵiriwo naŵabisa, motero adayankha kuti, “Zoonadi kunyumba kwanga kuno kudaabwera anthu ena, koma kumene ankachokera, sindikudziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;