Joshua 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangochoka anthu otumidwa ndi mfumuwo kutuluka mumzindamo, chipata chidatsekedwa. Ndipo adapita ku mseu kukaŵafunafuna azondiwo, mpaka adakafika ku dooko la Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthumwi za mfumu zija zitatuluka ndipo chipata chinatsekedwa. Nthumwizo zinapita kukawafunafuna azondi aja mpaka ku dooko la Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordano yomka kudooko; ndipo ataturuka akuwalondola, anatseka pacipata.