Joshua 20:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyo, nakafika pa malo achiweruzo amene ali pa chipata cha mzindawo. Atafika, asimbire atsogoleri mlandu wakewo. Apo atsogoleriwo adzamlola kuloŵa mumzindamo, nadzampatsa malo oti azikhalako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa chipata cha mudziwo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.