Joshua 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wofuna kulipsirayo akamlondola komweko, anthu amumzindamo asampereke munthu wopha mnzakeyo. Koma amtchinjirize chifukwa adachita zimenezo mwangozi, pakupha Mwisraele mnzake. Sadachite zimenezo mwachiwembu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.