Joshua 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adzakhala mumzindamo mpaka ataweruzidwa pamaso pa anthu onse, ndiponso mpaka mkulu wa ansembe wa nthaŵi imeneyo atafa. Pamenepo munthuyo angathe kubwereranso kwao, kumudzi kumene adachoka mothaŵa kuja.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumudzi kwake, ndi nyumba yake, kumudzi kumene adathawako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.