Joshua 20:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuvuma kwa Yordani, m'mapiri aja a kuvuma kwa Yeriko m'chipululu muja, adapatula Bezeri pakati pa mizinda ya fuko la Rubeni. Pakati pa mizinda ya fuko la Gadi ku Giliyadi adapatula Ramoti. Ndipo pakati pa mizinda ya fuko la Manase ku Basani adapatula Golani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani m'Basani wa fuko la Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'cipululu, kucidikha, wa pfuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Gileadi wa ofuko la Gadi, ndi Golani m'Basana wa pfuko la Manase.