Joshua 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraele onse, ngakhalenso alendo amene ankakhala pakati pao. Aliyense wopha munthu mwangozi, osati mwadala, ankatchinjirizidwa kumeneko. Womlondola kuti amlipsire sankaloledwa kumupha munthu wothaŵayo, mlandu wake usanazengedwe pamaso pa mpingo wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, kuti athawireko ali yense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.