Joshua 21:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina atsogoleri a mabanja a fuko la Levi adabwera kwa wansembe Eleazara, kwa Yoswa, mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akuru a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazare wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akuru a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli;