Joshua 21:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adaŵapatsa mzinda wa Kiriyati-Ariba. (Araba anali bambo wa Anaki), dzina lake linanso ndi Hebroni. Mzindawo unali m'dziko la Yuda lamapiri lija, pamodzinso ndi mabusa a zoŵeta kuzungulira mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawapatsa mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anoki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ace ozungulirapo.