Joshua 21:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe minda ya mzindawo pamodzi ndi midzi yake yomwe, adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune, kuti ikhale choloŵa chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yace.