Joshua 21:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho midzi yonse imene ili m'munsimuyi, adaipatsa zidzukulu za Aroni wansembe. Poyamba Hebroni, umene unali mzinda wopulumukiramo aliyense woimbidwa mlandu wa kupha mnzake mwangozi, pamodzi ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, ndiponso Libina,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzace, ndi Libina ndi mabusa ace;