Joshua 21:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ageresoni, gulu lina la fuko la Levi, adalandira mizinda iŵiri kuchokera ku theka la Manase wakuvuma: Golani ku Basani, mzinda wopulumukirapo munthu wopha mnzake mwangozi, ndi Besetera, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; midzi iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwiri kuchokera ku theka la Manase wa kummawa, Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapatsa ana a Gerisoni, a mabanja a Alevi, motapira pa pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo; ndi Beesitera ndi mabusa ace; midzi iwiri.