Joshua 21:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabanja a Kohati ndiwo anali oyambirira kupatsidwa mizinda. Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aroni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maere anaturukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa pfuko la Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.