Joshua 21:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaŵapatsa mtendere pakati pa anthu ena onse oŵazungulira, potsata zomwe Iye adaalonjeza makolo ao. Panalibe ndi mmodzi yemwe mwa adani ao amene adatha kugonjetsa Aisraele, chifukwa choti Chauta adaŵapatsa mphamvu zopambanira adani ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.