Joshua 22:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo atafika ku Geliloti, malo omwe anali pambali pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Kanani, adamangako guwa lalikulu ndi lokoma pambali pa mtsinjewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Geliloti, malo amene ali mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani mʼdziko la Kanaani, fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase anamanga guwa lansembe lalikulu pamenepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordano, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordano guwa la nsembe, guwa lalikuru maonekedwe ace.