Joshua 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele ena onse adauzidwa kuti, “Tamvani! Anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase adamanga guwa ku Geliloti m'malire a dziko la Kanani, tsidya lakuno la Yordani, moyang'anana ndi Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pamene Aisraeli ena onse anawuzidwa kuti anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a Kanaani ku Geliloti, ku tsidya lathu lino la Yorodani,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordano, ku mbali ya ana a Israyeli.