Joshua 22:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Finehasiyo adapita pamodzi ndi akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraele. Aliyense mwa akuluakulu amenewo anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafukowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi Finehasiyo anatumiza akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraeli. Aliyense mwa akuluakulu amenewa anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafuko a Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mapfuko onse a Israyeli; yense wa iwowa ndiye mkuru wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israyeli.