Joshua 22:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu onse a Chauta alikufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mwachimwa chotere, potsutsana ndi Mulungu wa Israele? Mwapandukira Chauta ndi kutsutsana naye pakudzimangira guwa limeneli, ndipo simukumtsatanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Gulu lonse likukufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwachita chinthu chonyansa chotere potsutsana ndi Mulungu wa Israeli? Nʼchifukwa chiyani mwapatuka ndi kuleka kutsata Yehova podzimangira nokha guwa lansembe? Mwapandukiratu Yehova!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utero msonkhano wonse wa Yehova, Colakwa ici nciani mwalakwira naco Mulungu wa Israyeli, ndi kumtembenukira Yehova lero line kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?