Joshua 22:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero tsono, ngati dziko lanulo ndi losayenera kupembedzeramo, pitani uko ku dziko la Chauta komwe kuli chihema chake chija, ndipo mugaŵane nafe dziko lathulo. Koma musapikisane ndi Chauta kapena kutisandutsanso ochimwa ife, podzimangira guwa lina kulimbana ndi Chauta, Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati dziko limene inu mwatenga ndi loyipitsidwa, bwerani ku dziko la Yehova kumene kuli chihema chake kuja, ndipo mukhale nafe limodzi. Koma inu musawukire Yehova kapena kutisandutsa ife kukhala opanduka podzimangira guwa lansembe, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukayesa dziko La colowa canu ncodetsa, olokani kulowa m'dziko lacolowaca Yehova m'mene cihemaca Yehovacikhalamo, nimukhale naco colowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.