Joshua 22:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati sitidamvere Chauta pamene tidadzimangira tokha guwa lopserezapo nsembe, kapena kumapereka zopereka zatirigu kapena zopereka zamtendere, Chauta yekha ndiye atilange.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, achifunse Yehova mwini wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati tinapandukira Yehova ndi kuleka kumutsata pamene tinadzimangira guwa loti tizipserezerapo nsembe kapena kupereka nsembe zaufa, kapena nsembe za mtendere, Yehova yekha ndiye atilange.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, acifunse Yehova mwini wace;